Katswiri wina oyimba nyimbo za uzimu M’dziko muno “Miriam Kuseni” wati wakonzeka kutulutsa nyimbo ina yatsopano m’mwezi omwe uno wa January.
Pakadali pano ndikuphikaphikabe kuti ndiwabweletsere zokomazi a Malawi
Kuseni
Polankhula ndi katswiriyu wati mutu wa nyimbo yomwe akuyembekezera kutulutsa ndi “Sanakhale Chete Yehova” yomwe itulukenso pamodzi ndi nyimbo yowonela.
“Pakadali pano ndikuphikaphikabe kuti ndiwabweleletsere zokomazi a Malawi”, “adayankhula motero “a Kuseni”
“Ndikuwalonjeza a Malawi kuti nyimbo zina zabwino za Miriam zikubwera ndithu zomwe zitsitsimutse miyoyo yawo ndipo adalitsika nazo” “adawonjezera kulankhula motero Katswiriyu”
Ndikuwalonjeza a Malawi kuti nyimbo zina zabwino za Miriam zikubwera ndithu zomwe zitsitsimutse miyoyo yawo ndipo adalitsika nazo
Sister Miriam Kuseni adayamba kuyimba m’chaka cha 2008 atatulutsa chimbale chake choyamba chotchedwa “Osaleka Kuyenda ndi Yesu”
M’chaka cha 2011 oyimbayu adabwelanso ndi chimbale china chachiwiri chotchedwa “Yesu ndi wabwino” chomwe chidamupangitsa kudziwika kumtundu wa A Malawi pa nyimbo yotchedwanso Yesu ndi wabwino. Izi zidapangitsa a Kuseni kuyitanidwa ndi Azungu kukayimba ku Mangalande m’chaka cha 2012.
M’Chaka changotha cha 2022 Sister Miriam Kuseni adatulutsa Chimbale chotchedwa “The Best of Sister Miriam Kuseni” chomwe chinakhazikitsidwa ku Nsungwi CCAP Church pa 30 October. Oyimbayu akuyembekeza kupanganso show ina chaka chino cha 2023.
Ndikuyembekeza kupanganso show chaka chino cha 2023
Mirriam Kuseni amagwira ntchito M’boma ngati Accountant ndipo amakhala ku Area 25 mum’zinda wa Lilongwe.
Article by Harris Msosa