Given Mulenga anabadwa pa 12 February m’chaka cha 1992 ndipo ndiwachiwiri kubadwa m’banja la ana atatu.
Kuyimba anayamba mu chaka cha 2018.watulutsapo chimbale chimodzi mutu wake “Chomwe Wadzala”.Choyamba nyimbo zanga zinayamba kubwera kumaloto nditatembenuka mtima kumene 2006 kenaka tinayamba choir yotchedwa Chaba Youth Assembless of God, kenaka kumayesela pa ndekha zinapezeka kuti zayamba kutheka kenaka ndinapanga chisakho chopita ku studio kuyamba kuyimba adatero Given.
Given amakhala ku dedza T/A chilikumwendo ndipo amagwira tchito ku Malawi Assembless of God Church ngati M’busa komaso ndi mlimi wa mbewu.