Lonnex Lawson Jeke Phiri anayamba kuyimba m’chaka cha 1993 pomwe anali ndi zaka 11. Mu chaka cha 2020 anatulutsa Album yotchedwa Ndiosunga moyo wanga.
“Ndinayamba kuyimba chifukwa chosangalatsidwa ndi mayimbidwe thawi imeneyo koma pano cholinga chenicheni ndikufalitsa uthenga wa Mulungu.” Adalankhula motero a Jeke.
“Chinthu chomwe ndikufunitsitsa kwambiri ndikutsekula Maso a anthu ambiri chifukwa anthu ambiri akukanabe zoti tili m’masiku otsiliza”.Adapitiliza kuwonjezera moteromo a Jeke.
Pakadali pano a Lonnex Jeke ali mu studio kujambula chimbale chawo chachiwiri chomwe chikujambulidwa ku B4P Studio komanso KB Studio kupatula akubwera Jehovah yomwe anajambula ndi Wells Ku Wells Studio ndipo kukakhala kotheka chaka chikubwerachi akhala akuchikhazikitsa chimbalechi.Lonnex Jeke pakadali pano akukhalira ku Tembisa Johannesburg m’dziko la South Africa.