Praise Nkwezalamba anabadwa pa 21 November, 1985 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 7, iye ndi wachitatu kubadwa ndipo amachokela m’mudzi mwa Nkoma pafupi ndi ku green corner mumzinda wa Blantyre.
Kuyimba anayamba mkale pamene anali ndi zaka 15 koma kuyimba payekha anayamba mu chaka cha 2019 ndipo ali ndi chimbale chimodzi chotchedwa Moyo Wanga Usakaiwale chomwe anachikhazikitsa pa 5 June 2022 ku Johannesburg, m’dziko la South Africa.Praise amachokera ku Chilobwe ku Blantyre koma pakadali pano akukhalira m’dziko la South Africa.