Nathan Simba anabadwa pa 28 June m’chaka cha 1989 lachitatu pa Chipatala cha Mangochi.
Nathan anayamba kuyimba pakathawi zedi koma amkayimba mu choir ndipo analowa mu studio m’chaka cha 2019, 2021 komanso chaka chino cha 2023 ngati choir ndipamene amamva kut Mulungu ali naye cholinga.Nathan kuyamba kuyimba yekha wayamba chaka chomwechino cha 2023 ndipo pakadali pano watulutsako nyimbo ziwiri zotchedwa Baba mwayenela komanso Yesu amamasula zomwe zajambulidwa Ku Many More Studio ndi Sam Guduza.
Sam amachokera ku Mangochi ku dela la Monkey Bay koma pakadali pano akukhalira ku Durban m’dziko la South Africa komwe akugwira ntchito ngati Uber driver.