Emmanuel Liwotcha anabadwa pa 7 July, 1977 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 11 atsikana 4 ndi anyamata 7 ndipo pano anatsala anyamata 5 ndi atsikana atatu kamba koti enawo anamwalira ndipo iye ndi wa namba 9 kubadwa ndipo amakhala ku area 23 ku Mount Molia mu mzinda wa Lilongwe.
Emmanuel anayamba kuyimba mu chaka cha 2010 ndipo anayambila kuyimba mu choir pa St Louis Montfort Parish pa Balaka komanso akuchokera ku banja la oyimba Isaac Liwotcha yemwe ndi m’chimwene wake.Mu chaka cha 2022 a Liwotcha anatulutsa nyimbo zitatu monga Mutichitile Chifundo,Mutimvele komanso Muyende Nane.