Albow Banda yemwe amadziwika bwino ndi dzina lakuti Albow B pamayimbidwe anabadwa mu chaka cha 1988 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana anayi ndipo iye ndi oyamba kubadwa.
Albow anayamba kuyimba m’chaka cha 2011 ndipo kufikira pano ali ndi zimbale zitatu monga Ndi Yesu Ameneyi, Mwamanga Pachani? komanso Ayoba ndipo pakatipa watulutsa nyimbo zina zatsopano zomwe zilipo 6 ndipo mayina a nyimbozo ndi monga Ndaimika Kaye, Come and see, Jerusalem iwe, Azakupeza uli pamwamba , Achulukilenji? komanso Dance and Joy.
AIbow amachokela ku Nguludi m’mudzi mwa Mataka T,A Likoswe m’boma la Chiladzulo ndipo pakadali pano akukhalira m’dziko la South Africa.