Precious Walfred ndi m’modzi wa oyimba nyimbo zauzimu yemwe anabadwa pa 25 December m’chaka cha 1997.
Precious wayamba kuyimba chaka chomwechino cha 2023 kudzela m’mayitanidwe a maloto.Precious watulutsa chimbale chake chomwe chikutchedwa Mwayenela Matamando chomwe chajambulidwa ndi Peter Michael Pemba ku Criss Media ndipo Ife tonse tiyamika ndi nyimbo imodzi mwa iyo yomwe ikupezeka muchimbale chatsopanochi.
Precious ndi mwana wa nambala 5 mu banja la ana 6 ndipo amachokera m’dera la Bangwe ku Blantyre ndipo pakadali pano akukhalira ku Cape Town m’dziko la South Africa.