Wyson Lubelo anabadwa pa 6 September, 1985 ndipo kwawo anabadwako ana 8, amuna anayi,akazinso anayi ndipo iye ndiwachiwiri pakubadwa.
Kwawo kwa Wyson ndi ku Mulanje T/A Mabuka m’mudzi mwa Chimwaza koma pakadali pano akukhalira m’dziko la South Africa.
Wyson anayamba kuyimba mu chaka cha 2007 koma chifukwa cha zovuta zina luso linkangoponderezeka chifukwa chosowa sapoti ndipo anadzakhazikika mu 2016. Wyson adatulutsa chimbale chake chotchedwa Chikondi Cha Ambuye mu 2019 chomwe adachikhazikitsa ku
Boksburg m’dziko la South Africa.