Samson Chapo anabadwa m’chaka cha 1991 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana asanu ndipo iye ndi oyamba kubadwa ndipo akukhalira ku Mponela,Dowa.
Sam anayamba kuyimba mu ma 90’s koma kuyamba kujambula nyimbo ku studio ngati oyimba anayamba mu 2019 ndipo kufikira pano Sam anatulutsapo chimbale chimodzi chotchedwa Nokha chomwe anachikhazikitsa pa 5 June 2022, ndipo pakadali pano akujambulanso chimbale chake china chachiwiri koma ngakhale izi zili chomwechi Sam anatulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa Mu Jesu mu mwezi wa January chaka chomwechino.
Kupatula kuyimba Sam amagwila ntchito ngati mlangizi wa WASH ku bungwe lina lalikulu M’malawi muno komanso Africa.