Ruth Chijani Zaipa anabadwa pa 24 May 1984, kwa bambo anabadwa ana awiri ndipo kwa mayi anabadwa ana asanu ndi m’modzi atsikana okhaokha ndipo konseku iye ndi oyamba kubadwa.
Anayamba kuyimba ali wachichepele mu ma choir a Sunday school kufikira kukula ndipo wakhala akuyimba mu ma choir ndi ma praise team osiyanasiyana.
Chidwi choyamba kuyimba ngati solo artist chidayamba kumufikila atabadwanso mwatsopano ndipo mu chaka cha 2023 ndi pamene anakwanilitsa kutulutsa chimbale chake choyamba chomwe mutu wake ndi “Amayankha” yomwe ili pa DVD komanso CD.
Pakadali pano Ruth akukhala mu dziko la South Africa komwe akugwila ntchito ndipo chimbale chake chimenechi watulutsira ku South Africa konko ndipo adayikhazikitsa kale ndipo iye adati pali maganizo okakhazikitsanso chimbalechi chaka chino m’dziko lino la Malawi.Pakadali pano Ruth ali ndi ganizo lofuna kutulutsa chimbale chake chachiwili zikayenda bwino mwa mphamvu ya Ambuye.