Rabson Mchizi anabadwa pa 18 December 1995 ndipo ndi oyamba kubadwa m’banja la ana asanu.
Rabson anayamba kuyimba mu chaka cha 2012 ndipo anayamba kuyimba nthawi imene amayimba mu choir ndipo choir master ataona kuti ali ndikuthekela koti akhoza kuyimba anamulimbikitsa ndipamene anaona kuti atha kuyimba.
Rabson ali ndi ma album awiri omwe anatulutsako yomwe imodzi anayimba ndi choir yotchedwa Mayankho pomwe ina anayimba yekha yotchedwa Bwenzi Lenileni ndipo Rabson amakhala ku Mzimba ndipo amapanga business.