Pastor Paul Chidothi amakhala mu mzinda wa Blantyre ndipo amagwila ntchito ngati Medical Health worker (wachipatala) komanso M’busa wapampingo komanso ndi mlangizi wa za mabanja kwa omwe adalowako kale komanso amene akufuna kulowa kumene (pre and post marriage counselor komanso iwowa ndi a Health and fitness instructor.
Pastor Chidothi adatulutsako chimbale chawo choyamba chotchedwa Revival mu 2020 komanso chimbale chotchedwa Chiyembekezo mu 2022 ndipo padali pano akujambula chimbale chawo chachitatu chomwe muli nyimbo monga Wandikumbukira Yahwe,Amai yomwe ikufotokoza zomwe amai amadutsamo kwenikweni iwo amene ali pa kangaroo ndi pemphero kwa iwo.