Pastor Magret Nangwale anabadwa mu chaka cha 1982 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana asanu ndipo iwo ndi achitatu kubadwa ndipo amakhala ku Chiladzulu.

Pastor Nangwale anayamba kuyimba mu chaka cha 1999 ndipo anayamba kuyimba kukwaya komanso amakonda kukhala m’magulu amene amakonda kuyimba nyimbo za Mulungu kufikila pano pamene Mulungu anawatsegula maso kuti atha kumayimba ndikugawa uthenga wabwino kudzera m’mayimbidwe.
Pastor Nangwale anatulutsako chimbale chimodzi ndipo pakatipa atulutsakonso nyimbo zina ziwiri zatsopano.