Pastor Dr Maggie Maurice anabadwa pa 25 October, 1978 ndipo m’banja mwawo anabadwamo ana 6 ndipo iwo ndi omaliza koma ana atatu anamwalira ndipo anatsalanso atatu.
Pastor Maurice anayamba kuyimba mu chaka cha 2009. “Ndinayamba kuyimba nditalota maloto nyimbo yanga yoyambilira yotchedwa Mulungu weniweni amayankha ndi moto, ndinali mu nyengo yayikulu zedi yomwe pandekha sindikanadutsa koma Yehova anandiyankha ndipo yankho la Yevova linatseka pakamwa pa nyengo yo ndipo lero ndikumutamandabe Yehova kudzera mu nyimbozi” adatero Pastor Maurice.
Pastor Maurice ali ndi zimbale zinayi komanso ma singles 4 ndipo mitu ya zimbale zawo ndi monga Mulungu weniweni amayankha ndi moto, Watsegula, Ndivuukemo komanso Hymns ndipo ma singles ndi monga Watibadwila mwana, Zinthu zonse zichitira ubwino,Anakubala komanso Wamkachisi. Pastor Maurice amakhala ku Kawale 2 mumzinda wa Lilongwe.