Mike Wiseman Tembo anabadwa mu chaka cha 1989 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 8, atatu adamwalira ndipo iye ndi wa namba 7 kubadwa.
Mike anayamba kuyimba mu chaka cha 2005 koma kuyamba kulowa mu studio anayamba 2008. Pakadali pano Mike akuyembekezela kutulutsa chimbale chake chotchedwa Satana Wadabwa.
Mike amachokera ku Thyolo kwa T/A Bvumwe koma pakadali pano akukhalira ku Soweto m’dziko la South Africa.