Kelvin Maxwell anabadwa m’chaka cha 1994 ndipo m’banja lawo anabadwa ana asanu, amuna atatu, akazi awiri ndipo iye ndi wachinayi kubadwa.
Kelvin anayamba kuyimba mu chaka cha 2006 koma kuyamba kujambula nyimbo ku studio anayamba mu chaka cha 2021.
“Ndinayamba kuyimba kamba koti nthawi iliyonse ndikakhala chete pandekha m’mutu mwanga mukabwera nyimbo ndimakhala okakamizika kumayiyimba mowilikiza kufikila nditayiloweza nyimboyo ndipo ndimaloweza nyimbo popanda kuyilemba mpaka kufikila lero sindilemba nyimbo zimangobwera m’mutu mwanga, apa mpomwe ndinazindikila kuti ndikuyenera kunyamula uthenga wa Ambuye kudzera mukuyimba” adatero Kelvin.Kelvin sadamalize kujambula chimbale chake choyamba chotchedwa Gehena.
Kupatula kuyimba Kelvin amapanga business komanso amagwila tchito ndipo amachokera ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre koma pakadali pano akukhalira ku Durban m’dziko la South Africa.