Costance Faith Kapanda anabadwa pa 19 September, 1994 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 4 ndipo iye ndi womaliza.
Faith anayamba kuyimba m’chaka cha 2010 pamene adali ku sukulu ndipo pomufunsa funso kuti adayamba kuyimba bwanji faith adati “Ndidalota nyimbo kenako nkumaikumbukirabe nditadzuka ndinazindikira kuti Mulungu wandiululira career yanga”.Faith watulutsa chimbale chake chotchedwa Tiwoloka chomwe watulutsa mu mwezi wa January chaka chomwe chino.Faith amakhalira ku Mponera, Dowa ndipo ndi mphuzitsi wakusukulu yapulayimale.