Baxfull Joseph Nefutary (B. J. N) anabadwa pa 15 April, 1987 ndipo anayamba kuyimba mu chaka cha 2021.M’banja mwawo anabadwa ana 9 koma 5 adamwalira adatsala ana 4 ndipo iye ndi wachisanu pobadwa.
Baxfull adayamba kuyimba nthawi imene amakonda kumvetsera nyimbo kwambiri komanso panthawi yomwe adayamba kuyimba choir amatha kupeka nyimbo ndikumazipeleka ku choir kuja.
Pakadali pano Baxfull watulutsako nyimbo zokwana ziwiri za tsopano ndipo inayo inatuluka pa 07 March ndipo yapompanoyi wayitulutsa pa 09 April 2024.
Baxfull akukhalira ku Peitermalitzburg kufupi ndi Durban m’dziko la South Africa ndipo ku Malawi kuno amakhalira ku Mangochi kumakanjila kwa T/A Namabvi dera la mfumu a Kadango.