Oyimba nyimbo za uzimu otchuka m’dziko muno Khama Khwiliro watulutsa nyimbo yatsopano dzulo yotchedwa Testimony.
Nyimbo yatsopanoyi ikukamba zoyamikira Mulungu komanso kuthokoza kuti chipanda Yesu m’nali chabe koma moyo wanga wasintha chifukwa cha Yesu osati wina ayi ndipo nyimboyi yajambulidwa ndi OBK BEATS “adayankhula motero Khwiliro”
Ndikufuna nyimbo zanga angakhale zikapita ku International store ndizipeza nazo phindu chifukwa choti kunjako atha kunvela nkupanga download
Khama Khwiliro
Chaka cha 2023 chino ndakonzeka kwambiri ndipo nyimbo nde ndajambula zambiri nduchita kusowa kuti ikatha iyi nditulutse iti? Ma plan ndioti ndikukonzekela Show yanga yapamwamba yozaimba nyimbo pafupifupi 20..Chifukwa ndasinthanso kayimbidwe kanga muthanso kuona kuti kaimbidwe kanga kasintha..Ndikufuna nyimbo zanga angakhale zikapita ku International store ndizipeza nazo phindu chifukwa choti kunjako atha kunvela nkupanga download..Mu kuimba muli chuma koma timaphweketsa zinthu sitikhala ndichidwi m’chifukwa chake mayimbidwe athu sakupita patsogolo “adayankhula motero Khama.”
Khama Khwiliro adayamba kuyimba m’chaka cha 2000 koma adayamba kujambula nyimbo ndi gulu la Christ Melodies m’chaka cha 2004 pomwe adatchuka ndi nyimbo monga Khululukireni komanso Landitseni.
Khama ndi wachitatu kubadwa m’banja la ana asanu, amuna awiri ndi atsikana atatu ndipo akukhala ku Lunzu mum’zinda wa Blantyre komwe wamangako nyumba yake.
mutha kutenga nyimbo yatsopano ya Testimony ya Khama Khwiliro popita pa link ili m’musiyi
Article by:Harris Msosa