Oyimba odziwika bwino ndi nyimbo za uzimu m’dziko muno Henry Masamba watulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa Levoz yomwe wayimba ndi mwana wake Moriah.
Nyimboyi yajambulidwa ndi Macia ndipo ikukamba za ulemelero wa Mulungu kulimbikitsa munthu amene wataya chiyembekezo chifukwa nyengo zathina.Bible ku akorinto likunena kuti diso silinaone ndipo khutu silinanve zomwe yehova wawakonzera ana ake kotero ngati okhulupilira akhale nako kulimbika mtima kuti zinthu zikusintha ndipo sakhalaso chimodzimodzi yehova akutikweza kuchoka paulemerero Wina kupita pamwamba. “adawonjezera motero a Masamba.”
Masomphenya anga ndi ofalikira dziko lonse ndi uthenga wabwino kudzera m’mayimbidwe ndipo mu zaka 5 zikubwerazo ndikuziona nditakwaniritsa zimenezi
Henry Masamba
Masomphenya anga ndi ofalikira dziko lonse ndi uthenga wabwino kudzera m’mayimbidwe ndipo mu zaka 5 zikubwerazo ndikuziona nditakwaniritsa zimenezi “adayankha motero a Masamba poyankha funso loti masomphenya awo ndi otani.”
Henry Masamba akuthokoza onse okonda nyimbo zake ndipo akuwamema kuti apitilize kumusapota. Masamba wapemphanso onse okonda mayimbidwe ake kuti atha kumutsatira patsamba lake la facebook lotchedwa Henry Masamba popanga like.
Henry Masamba amakhala ku Kawale mum’zinda wa Lilongwe.
Mutha kutenga nyimbo ya Levoz ya Henry Masamba Featuring Moriah pa link ili m’musiyi
Article By:Harris Msosa