Oyimba nyimbo za uzimu odziwika bwino m’dziko muno Bon Kavala Banda wati watulutsa chimbale chake chatsopano chomwe chikutchedwa kuti pa Bill ya Yesu. A Kavala Banda ati Chimbalechi chili ndi nyimbo zisanu ndi ziwiri pakadali pano ndipo nyimbo zina zomwe zikupezeka m’chimbalechi ndi monga 3:0, mundione mawa, komanso pa bill ya Yesu. pakadali pano Bon watulutsa nyimbo yotchedwa mundione mawa yomwe ikupezeka pa website ya www.malawigospelmusic.com.
Bon_Kavala_Banda ndi oyimba yemwe adayamba kuyimba kale kwambiri m’chaka cha 2005 koma kuyamba kuyimba nyimbo za uzimu adayamba m’chaka cha 2013 pomwe adabwera ndi nyimbo ya nyengo zowawa yomwe idali m’chimbale chakenso chotchedwa Nyengo zowawa yomwe idatchuka kwambiri munthawi imeneyo.
Kupatula kuyimba Bon amachitanso za ulimi ndipo ndi mwana oyamba kubadwa m’banja mwawo. Bon ndi okwatira ndipo ali ndi mkazi ndi ana ndipo amakhala ku Area 23 mumzinda wa Lilongwe.
Article by Harris Msosa