Davie Ronald Chirambo anabadwa pa 6 June, 1988 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 6, akazi awiri,amuna anayi ndipo Davie ndiwachinayi kubadwa.Kumudzi kwawo ndi kwa T/A Mpherembe, m’mudzi mwa Msafire, boma la Mzimba, Davie ndi msilikali wa Malawi Defence Force ndipo amakhala ku Zomba.
![](https://www.malawigospelmusic.com/wp-content/uploads/2024/04/IMG-20240414-WA0024.jpg)
Davie anayamba kuyimba mu chaka cha 2003 koma anajambula chimbale chake mu 2016.
Davie anatulutsa chimbale chake chotchedwa Ndichisomo mu 2016 ku Groove Magic Studio kwa Malemu Joseph Tembo chomwe munali nyimbo zokwana 11 ndipo pakadali pano akujambulanso chimbale chatsopano chotchedwa Umfunse Yesu. Davie wajambulapo nyimbo zokwana 8 monga Umfunse Yesu, Kwa Yesu, Yendabe ndi Yesu, Alinkutsilizika, Ndilumirenji Mnofu Wanga, Sinzaleka komanso Mwayenera ndipo zina mwanyimbozi anayimba ndi oyimba monga Macdonald Indonga Kachingwe,Harold Singini komanso Benard Gwayi.