Middien Kanyika yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Middien 100% pa mayimbidwe anabadwa pa 10 October, 1992 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 8 ndipo iye ndi wa chi 7 kubadwa.
![](https://www.malawigospelmusic.com/wp-content/uploads/2024/04/IMG-20240417-WA0033.jpg)
Middien anayamba kuyimba mu chaka cha 2014 ndipo kufikira pano ali ndi chimbale chimodzi chotchedwa Chipatso cha Mzimu chomwe anachikhazikitsa pa 28 October, 2018 ku Johannesburg m’dziko la South Africa.Pakatipa Middien watulutsako nyimbo zina ziwiri zotchedwa Wapambana komanso Pa Mpando.
Kupatula kuyimba Middien amagwira ntchito ku ma bus a Matours International Coach Cross Border komanso amapanga business ya cosmetics, home wear komanso kugulitsa zovala zochokera mayiko akunja. Ku Malawi kuno Middien amakhala ku area 22 ku Lilongwe koma pakadali pano akukhalira ku Johannesburg m’dziko la South Africa komwe akugwirako ntchito.