Jolly Jack Chikaonda anabadwa pa 28 May, 1983 Ku mudzi kwawo ndi ku Luchenza (Municipal) boma la Thyolo,ndipo anayamba kuyimba kalekale cha m’ma 1998 koma kutulutsa nyimbo ngati oyimba wa nyimbo za uzimu chinali chaka cha cha 2014.
Mu Family yawo anabadwamo ana 10 ndipo iye ndi wa number 9 kubadwa.Kuyimba anayambira mu choir cham’ma 1998 ndipo kuchokera mu 2014 pomwe anayamba kuyimba Jolly watulutsako chimbale chimodzi chotchedwa Ayuda mu 2018.
Kupatula kuyimba Jolly amagwira ntchito ndi boma la Malawi ngati Mphunzitsi wa school ya primary.
Ku Malawi kuno chifukwa cha ntchito ndikumazugulira ndithu maboma ochuluka koma panopa ndikupezekera pa Ntaja Trading boma la Machinga ndikomwe ndikukhala adatero Jolly polankhula naye.
Pakatipa watulutsa ma single atatu Sindinjenjemera mu 2018, Yesu wabadwa mu 2019 ndi Konda dzina la Yesu mu 2024 koma kamba kosowa chuma sanakhazikitseko chimbale chake koma mtsogolomu malingaliro amenewo alipo ndithu adawonjezera kulankhula motero Jolly.