Monica Chidzere Banda anabadwa m’banja la mayi ndi bambo Chidzere, dzina la mayi ake linali Annie Stellia Chamanga a m’mudzi mwa Mphamba Machenga T/A Njewa. Abambo ake dzina lawo anali Mgiyo Chidzere a M’mudzi mwa Mkwayira T/A Njewa.Abambo ake anamwalira iye ali wang’ono sanawawoneko ndipo anakula ndi mayi komanso za chisoni amayi akewonso anamwalira mchaka cha 1996.
Monica C. Banda anabadwira ku Bottom Hospital ku Lilongwe pa 15 August,1983 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 6 koma adatsala amoyo 5, mwana m’modzi adamwalira ndipo iye ndi omaliza wa number 6 pobadwa.Atangobadwa anapatsidwa dzina loti Monica ndipo atabatizidwa sanasitheso dzina.
Mayitanidwe amayimbidwe adamufikira ali wachichepele kwambiri komaso samangokhala ayi amayimba nawo choir ya azimayi ya Kingdom Gospel Church, koma kufika pa air wayamba kupezeka chaka chomwe chino cha 2024 chomwe watulutsa Extended Playlist yake yotchedwa “Ndikumbukireni” ndipo ali pa banja komanso adadalitsika ndi ana 4 amuna awiri,akazi awiri omwe mayina awo ndi Havillah Beatrice Banda, Stellia Annie Banda, Collings Steve Banda komanso Wisdom Banda kuphatikiza apo amapangaso za u MC ndipo dzina lake lodyera ndi Zayaweh.