The servant of God Mirriam Chipwaila anabadwira ku Mangochi kwa Mfumu Katuli,pachipatala cha Chigweje.Anabadwa pa 26/09/1986 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 9 akazi asanu ndipo amuna anayi.The servant of God ndi wa nambala 5 pobadwa.
Atangobadwa adapatsidwa dzina loti Dyles ndipo atabatizidwa adamutcha Mirriam.Maitanidwe amaimbidwe adamufikira ali wachichepere ndi zaka zosachepera 15 pomwe adakayamba kwaya ya The sodgers of the king pa St Luke ,Liwaladzi Anglican Church,m’boma la Nkhotakota.Mirriam adakhala odalilika pa utumikiwu kufikira kukula ndipo mu chaka cha 2019 The servant of God Mirriam Chipwaila ndipomwe adayamba kujambula nyimbo ndipo kufikira pano ali ndi chimbale chimodzi chomwe mutu wake ndi Adzatimenyera Nkhondo.
The servant of God, Mirriam Chipwaila ndi mzimai yemwe wadutsa munyengo zolimba ndipo kukhala ndi moyo ndi umboni waukulu,iyeyu anadalitsidwa ndi ana awiri akazi okhaokha.