Home » THE DEVIL CHALLENGERS/AKUNAMA BOYS – BIOGRAPHY

THE DEVIL CHALLENGERS/AKUNAMA BOYS – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
386 views

The Devil Challengers ndi gulu lomwe muli anyamata oyimba awiri ndipo anyamata amenewa mayina awo ndi Joel Majuni komaso Elijah Njirayagoma.

Joel ndi ochokera m’mudzi mwa Rhoda mfumu yayikulu Kunthembwe/Chileka boma la Blantyre ndipo ndi mwana oyamba kubadwa m’banja la ana atatu akazi awiri ndipo anakwatitsa ukwati wake PA 15/October /2021 ali ndi ana awiri Sylvester ndi Trace.

Elijah Njiragoma ndiochokera m’mudzi mwa Makwangwala mfumu yayikulu Kwataine boma la Ntcheu ndipo ndi mwana wachiwiri kubadwa mu banja la ana asanu ndipo m’mbanjamu anabadwa amuna anayi mkazi m’modzi ndipo ndi okwatira ali ndi mwana m’modzi wa mkazi Testimony.

Joel komaso Elijah ndi oyimba omwe akhala akuyimba pa yekha pa yekha asanakumane koma kuchokera mu chaka cha 2017 ndipamene anapalana ubale pomwe anakumana mu mpingo wa Disciples Assembly Church ndipamene anapanga ubale wawo ndikuyamba kuyimbira limodzi.

2019 analowa mu studio komwe anatulutsa nyimbo yotchedwa Akunama,nyimbo imeneyi amamuuza poyera Satana kuti wachepa ndipo ndiwolephera ndipo nyimbo iyi anthu anaikonda zedi ndipo 2021 ndipamene anatulutsa video ya nyimbo imeneyi ya akunama.

Sanalekere pomwepo 2022 anaphikabe nyimbo ina yomwe ndi Chibomba cha mapemphero yomwe ikufotokoza za nkhondo zomwe timakumana nazo zomwe paife tokha sitingathe kutulukamo chifukwa timakhala kuti tazingidwa tili mu linga la adani nde ndipephero lokha lomwe lingatipulumutse.Pa 7 December, 2023 anatulutsa video ya Chibomba cha mapemphero kotero pakadali pano ikutumikiranso nyimbo imeneyi.

The Devil Challengers yayimangati asilikali omwe akulimbana naye oyipayo komaso akuyimba nyimbo zolimbikitsa kuti pamene tikumana ndi mayesero tisataye mtima.

Pakadali pano ali mu studio komwe akukonzekeranso kutulutsa nyimbo yotchedwa Yakwana nthawi yomwe apanga feature Kondwani Chirwa ndipo maitanidwe awo amalemekeza aliyese mpingo uli onse.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media