Shard Haakim amachokela m’boma la machinga…ku Ntaja…moti anabadwa pa 14 January 1979.
CHIYAMBI CHAMAIMBIDWE
Muchaka cha 2013 anayamba kudwala matenda osaziwika bwino bwino Kupita kuchipatala amati sakuona thenda iliyonse moti anazuzika kwa 3 years kudwala kwa serious …pofika athu kumamuwengela masiku kuti kucha kwa mawa uyu Safika ….
usana ndi usiku osagona ululu okhaokha.Moti ataona kuti zamoyo palibe 12 koloko ya usiku ..anakhala akuzilingalira mtunda umene ayenda ndi thenda yawo… zinawakhudza kwambiri poganiza kuti achoka nao kutali ndipo palibe chikusitha ayenda kwasing’anga kukanika…kwa prophet kukanika …azibusa osiyana siyana palibe.. zipatala palibe.. ndalama kumangonongeka anangoona kuti apa kwawo kwatha basi…
Ndipo anaganiza kuti atenge moyo wawo ndikuwupeleke m’manja mwa Mulungu podziwa kuti moyo ndiwake….anatseka maso ndikupephera mosweka mtima ….pephero lalifupi kwambiri koma linachita zithu zazikulu kumoyo wawo….anati ambuye choyamba mulandile ulemu ….thenda imene ndikudwalayi ngati mukuona kuti sindichila ndikupephani tsiku la mawa ndisalione koma ngati mu kuona kuti ndichila ndichizeni …pephero lawo linathela pamenepo.Moti atangomaliza pephero lawo anagona tulo usiku omweo …moti sanayambe agonapo chiyambire moti anadzuka 11 koloko yamasana chigonele cha usiku.
Atangodzuka anaona thupi lawo kupepuka moti sanali kuyenda koma tsiku limeneli anadzuka kuyenda kuchila kunali komweko
ndiye ataona kuti achila anali kusakasaka chithu chimene angathe kumuthokoza nacho Mulungu pazimene wawachitila…..anagona usiku analota kumwamba kutatsekuka kunatuluka mawu ….akuti thawi yakwana yoti unditumikile …ndipo sanathe kumvetsesa bwino chomwe chimkatanthauzilidwa pathawi imeneyo ndipo anangoti kakasi kusowa chochita patchito imene anapasidwayo anali asayambe ayichitapo. Akusikhasikhabe kumaloto komweko anadzidzimuka ndipo anapephela atangomaliza kupephela thawi yomweyo anayimba nyimbo zokwana zitatu usiku omwewo…m’mene kunkacha kum’mawa ali ndi nyimbo zokwana zitatu zoveka bwino zokhuzaso kwambiri moyo wawo
Pamenepo ndipamene anaona kuti kuyamika kwawo kukhale kuyimba nyimbo za gospel.
2018 ndipamene anatulutsa album yawo yoyamba yotchedwa yehova wanga….zinali zowakhuza kwambiri palibe chimene anachiona kuti chakwanila pamaso pa Mulungu pakumuyamika kwawo…..anakhalaso zikuwawawa kwambiri kuti kuyamika kwawo sikukukwanila pamaso pa Mulungu….panaliso tsiku lina anagona analota ali mutchalitchi akutumikila …zimene zinachitika kokwana masiku atatu mowilikiza…atasikhasikha anaona kuti awa ndimaitanidwe okuti ayambe kumutumikila…kutacha kumawa anayitana athu amene anali maneba awo ndipo anapemphela nao kenako analowa m’mawu kuyamba kutumikila moti zomwe zinachitika kumaloto zija zinachitikaso pamalo pamenepo, panali zamphavu ma deliverence anali Pamenepo…mpingo unayambika tsiku limelo moti kuyambila tsiku limenelo dzina lawo linasitha..anayamba athu kuwatcha Abusa moti panopa ndi oyimba koma ndi M’busa…
Palibe chomwe sanaleke zamaimbidwe anali akupitilizabe mpaka kuzatulasa chimbale chotchedwa SOLDIERS OF GOD.