Sella Chirwa anabadwa mu chaka cha 1997 pa 22 November ndipo ndi obadwa mu banja la bambo Ragson Kamunda Chirwa ochokera ku Nkhatabay ndi mayi Mary Kusupa ochokela ku Chikwawa ndipo ndi wachinayi kubadwa mu banja la ana 5.Anayamba kuyimba mu Chaka cha 2020 ndipo anatulutsa nyimbo zitatu monga Ndinu Zonse zanga, Mundikondetsetsa,Ndine wake wake Produced by sir encious
Sella anayamba kuyimba ali kamwana ku kwaya ndipo anazindikila mayimbidwe ake atakwatiwa mu Chaka cha 2015 ndi Emmanuel Paul Kalilitu ndipo ali ndi ana awili atsikana.
Mu Chaka cha 2023 watulutsa nyimbo 4 monga Ndapatsidwa mphamvu,Mkazi wangwiro,Yesu ndinu oyela komanso Yesu mwamuna wantanda Produced by Michael Pemba (zoom media).