SAMUEL SONGEYA NDI M’NYAMATA WOCHOKERA M,BOMA LA NTCHEU T/A INKOSI NJOLOMOLE,GV MUWALO CHAULUKA VILLAGE , GOWA MISSION
SAM ANABADWA PA 01/09/1990 PA QUEEN ELIZABETH HOSPITAL (QUEENS )MU MZINDA WA BLANTYRE
PANTHAWI IMENE BAMBO AKE A SAM A FRIEZER S. SONGEYA OMWE AMACHOKELA M’MUDZI WA KAMPANJE T/A GANYA M’BOMA LOMWELO LA NTCHEU AKUKHALA KU CHILIMBA PAMODZI NDI A MAYI A PASTOR STELLAR NYAMBO ABUSA AMPINGO WA BELIEVEREN CHRIST.
SAM ANABADWA MU BANJA LA ANA ANAYI ANYAMATA ATATU MTSIKANA M’MODZI NDIPO IYE NDI MWANA WA CHISAMBA .IYE WAKULILA MADELA OCHULUKA CHIFUKWA BAMBO AKE NDI APHUNZITSI AKU PRIMARY.
ANACHITA MAPHUZILO AKE ASUKULU YA PRIMARY MASUKULU ANGAPO MONGA CHIKAPA ,NTCHAUYA LINKHUWE , MUWALO , GOWA KOMASO KAMPANJE,SUKULU YAKE YA SECONDARY WAPHUZILA PA KAMPANJE CDSS.SAM NDI KHRISTU WOBADWA MWATSOPANO YEMWE ANABATIZIDWA MU MPINGO WA CHURCHES OF CHRIST IN MALAWI GOWA SYNOD NDI ABUSA A T .SUYA OMWE ANALI A MODERATOR PA GOWA MISSION M’CHAKA CHA 2015 ,NDIPO KUFIKA PANO NDI NKULU WAMPINGO WA MUWALO BRANCH.
SAM NDI NDIMUNTHU WOKONDA KUYIMBA AMAKONDA KUYIMBA NYIMBO NDI MAYI AKE AKAKHALA KU MUNDA NDIPO MAYI AKE AMAMVA KUKOMA AKAMAWAVOMELEZA.IYE ANALOWA MU MUSIC MINISTRY M’CHAKA CHA 2019 ATATULUTSA NYIMBO YAKE YOYAMBA YOTCHEDWA (MWALIKONDA DZIKOLI) NDIPO ANTHU ANAZINDIKILA KUTI MWA IYE MULI UTUMIKI NDIPO ATAPANGA PERFORM PANSONKHANO WA UKULU WAPACHAKA WA CHURCHES OF CHRIST KU DWANGWA. ANTHU AMBIRI AMAMUTCHULA KUTI MR GOOD NEWS CHIFUKWA CHA NYIMBO ZAKE ZOGWILA MTIMA.