Ruth Chijani Zaipa anabadwa pa 24 May 1984 kwawo kochokela ndi ku Kasungu east kwa T,A Wimbe kwa Chamama. Ali pa banja ndi ana atatu.
Chidwi chakuyimba adayamba ali wachichepele pomwe ankayimba mu ma choir a ku church ( Sunday School Choir) pa Thumba CCAP kwa Chamama. Kuchokela nthawi imeneyo wakhala akuyimba ma choir osiyanasiyana ku Secondary School komanso ma church choir.
Chidwi chofika poyimba as a solo artist chidalimbikitsika atakula komanso atabadwa mwatsopano.Pakadali pano watulutsa album imodzi yomwe mutu wake adayitcha Amayankha yomwe adatulutsa mu 2023 DVD komanso CD ndipo zonsezi watulutsila ku Johannesburg South Africa. Audio anapanga direct ndi Fanuel Holyup pomwe DVD anajambula komanso kupanga direct ndi Jack Jonas Pakadali pano ali pa project yofuna kutulutsa album yachiwili.