Precious anabadwira pachipatala cha Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre,nthawi imeneyi mkuti makolo ake akukhala mdera lotchedwa chilimba.Precious ndi namba 3 pakubadwa ndipo m’banja mwawo alimo ana 6 amuna awiri, ndi atsikana 4,ndipo anasamuka ku chilimba ndikupita ku Ndilande komwe anamangako maziko makolo ake.
Precious anayamba kuyimba ali wachichepele ku Church yotchedwa CHURCHES OF CHRIST ndipo amayimba mu church Choir yotchedwa Galileya Choir ku ndilande komweko.
Pakadali pano Precious ali ku South Africa komwe akugwira ntchito ndipo kumeneko ndi m’modzi mwa anyamata amene akumakhala busy kwambiri maka kumbali yama backing vocals, ndipo iye ali busy kukazinga nyimbo zake mwa ina yomwe anayimba yomwe yavuta ndiyoti Mwayenera yomweso ikupezeka pa website yayikulu ya Malawigospelmusic.com.