Platson Keliam Chammudzi anabadwa ndi kukulira ku Neno m’mudzi wa amtemankhawa T/A Dambe.Platson anabadwa pa 5/01/1994 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 8 anatsala amoyo 7 m’modzi adamwalira ndipo iye ndi wa number 3 pobadwa.
Atangobadwa adapatsidwa dzina loti Platson ndipo atabatizidwa ku church sadamusinthe dzina koma kupitilira ndi dzina lomwelo kufikila pano.
Mayitanidwe amayimbidwe adamufikila ali wachichepele kwambiri koma kufika pa air adayamba kupezeka mu 2019 pomwe adatulutsa nyimbo yake yotchedwa Chingalawa cha Nowah ndipo iye ali pa banja komaso adadalitsika ndi ana awiri amuna maina awo ndi joseph ndi Rex platson.