Paul Phiri anabadwa pa 12 December 1997 ku Lilongwe pa chipatala cha Bottom.Paul ndiwoyamba kubadwa ku banja la malemu mai ndi bambo Phiri, pamutu pake panaponda ana 4 omwe m’modzi wa iwo anamwalira.Kondwani, Pemphero ndi Idrissah ndiwo ang’ono ake a Paul Phiri omwe alipo pakali pano.
Paul Phiri waphunzira sukulu ya primary pa Chatuwa Primary School,ndipo secondary yake wachita pa Bwaila Secondary School.
Paul Phiri anayamba kuyimba mu chaka cha 2019 ngati solo artist,koma mbuyomu wakhala akuyimba ku gulu loyimba nyimbo za matamando la ku kachisi komwe amapembedzerako.Pakadali pano Paul Phiri watulutsa chimbale choyamba cha nyimbo zomvera chotchedwa “Ndidikilira Pa inu” chomwe cha nyamula nyimbo 10 ndipo akuyembekezeka kujambula ma videos ake komaso kupanga launch mu 2024.Kupatula kuyimba Iyeyu amapanganso audio production ndipo chimbale chimenechi, Paul, anadzijambulira kuchokera ku AIM RECORDING STUDIO m’chaka cha 2019.
Khumbo la pa mtima pa Paul Phiri ndilo kutumikira Mulungu kwa mtundu wake (malawi) komanso mitundu ya anthu a maiko ena kuti Ambuye Yesu Khristu akakhudze miyoyo ya anthu ake kupsyolera mu luso la mayimbidwe lomwe Paul anapatsidwa.