Maria Lemani Banda anabadwa m’chaka cha 1985, anabadwira ku Nguludi Hospital ndipo ndi mwana wa number 5 ku banja la Mr and Mrs Lemani Dzonzi.Maria Lemani ndi okwatiwa ali pa banja ndipo chokhumba chake ndikufuna kufalitsa uthenga kudziko lonse kudzera mkuyimba ndipo Maria anapanga Theology ku Wings of Eagle Bible Collage ku Blantyre moti ndi m’busa.
Maria Leman amakhala m’boma la Mwanza ndipo iye ndi mulimi.Anayamba kuyimba m’chaka cha 2017,anatulutsa album yoyamba mu 2019 audio and DVD,chimbale chotchedwa Chimdalitso 2021 ndipo 2022 watulutsanso ma single atatu,1 Tachirowadi,2 Wabadwa ndipo yachitatu “Mutikumbuke” yokhudza Covid) ndipo nyimbo izi zakhala zikuyikidwa m’ma Radio komaso m’ma TV. Maria lemani sanayimbepo ndi munthu aliyense koma chisomo cha Yehova chinamugwera kumapeka nyimbo mkumatulutsa.
Tsopano Maria Lemani akufuna kutulutsa album yachiwili yotchedwa Zitembenuke yomwe audio ndi DVD zatha kale ndipo pa 1 september 2024 ikhala ikupangidwa launch ku Manza Hotel.