Nathan Simba was born on 28 June 1989 at mangochi hospital.Fourth born son in a family of five (Three boys and two girls.
Nathan Simba anabadwila ndi kukulila ku Mangochi M’mudzi mwa a Mwalembe ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 5 koma adatsala awiri, ana atatu adamwalira ndipo Nathan ndi mwana wa number 4 mu banja la Mr and Mrs Simba.
Nathan atangobadwa anapatsidwa dzina loti Nathan ndipo atabatizidwa anapatsidwa dzina loti Geofrey komano anthu sanakwanitse kapena kuti sanasithe linawasangalatsabe dzina loti Nathan and mpaka pano amayitanilidwabe Nathan.
Mayitanidwe amayimbidwe Nathan anamufikila pakathawi ndipo wayimbako ma choir mpaka pano ndi wa choir ina ku South Africa imene imatchedwa Ebenezer Church Choir ndipo Nathan Simba ndi choir master mu choir imeneyi.Nathan adalandila vumbulutso lomwe Mulungu anapeleka Kwa Mtumiki wina amene ananenelela pa moyo wa Nathan kuti munthuyu ndi oyimba ndipo Mulungu anamuyika pa dziko pano ndi cholinga ndipo akuyenela kut amutumikile Mulungu ndipo wakhala akulota ndipo Mulungu amamuyakhula ku tulo kuti mwana wanga ukuyenela kut unditumikile.