Home » NASHO NYIRENDA – BIOGRAPHY

NASHO NYIRENDA – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
214 views

Born on 25 February 1982 at Kasungu hospital,seventh born son of Mr and Mrs smart John Chisimba Nyirenda.Nasho ndi okwatira ndipo ali ndi ana awiri ndipo chikhumbokhumbo chake akufuna kufalitsa uthenga dziko lonse la Malawi mukuyimba.Nasho anaphunzira sukulu yake ku Manja Primary School ndipo Secondary ku Chichiri ndi Chinamwali ku Zomba anapanganso Marketing ndi Business and lndustrial Administration ndipo pakadali pano akugwira ntchito ku Puma Energy ngati sales technician.

Anayamba kuyimba mu choir ya family ali wachichepere 10years, atakula pang’ono anayambisa gulu lotchedwa Christ Melodies lomwe linali lapampingo pa St Columba CCAP,momwe munali iyeyo,Khama Khwiliro,Clement Nkhoma ndi Mbumba Mbewe.

Nasho Nyirenda anayamba kudziwika ngati solo artist in 2016 pamene anatulusa chimbale chotchedwa Zatheka nyimbo imene inawonetsedwa kwambiri mumakanema komanso kuyikidwa kwambiri m’ma radio.Nasho anakulira ku Blantyre ndi achemwali ake oyamba kubadwa ndipo Nasho ndiwomaliza wa number 7 mu nyumba ya mai ndi bambo Nyirenda.

Ngati woyimba anayamba kuyimba kalekale nthawi imeneyo magulu alipo atatu, yawo yotchedwa Christ Melodies,Springs and Adams family ndipo ma solo artist alipo Lloyd Phiri ndi abusa a Wyclif Chimwemdo,nthawi imeneyo ali ndi chimbale chotchedwa Mbuye khululukile ndi Landitseni.Kuyimba yekha ngati solo artist adayamba kuyimba in 2016 after atapanga launch album yawo yomaliza ngati gulu in 2013 yotchedwa wandilephera.Ngati woyimba ali ndi album imodzi koma pano he is working on another album yomwe itchedwe zatheka volume 2 yomwe zina mwa nyimbo zitapezeke m’menemo zinayamba kale kujambulidwa, ndipo zina zinatulusidwa kale ngati ma singles monga,Sagona tulo feat Barry Uno,Ndatola feat Reina and Mafo komanso Saka.

As an artist he was the first guy to feat Onesmus pa show yawo atangosintha kumene kuchokera ku circular music kufika ku gospel,nthawi imeneyo gospel music ikukoma ndipo atulutsapo number of songs zimene zachita bwino kwambiri pa Malawi pano ndipo Nasho akuyembekeza kumaliza zatheka volume 2 this coming year 2024.

Nasho ndi mkhristu wa CCAP ndipo ndi oyimba okhazikika ku mpingo umenewu.Nasho Nyirenda akuyembekeza kupanga launch album yake ikatuluka ndipo pakadali pano ali ndi ma producer atatu omwe akupanga za album yake monga,OBK,FOXY and Steve Mereka.Pakadali pano Nasho ngati oyimba ali nawo m’magulu ngati MUM ndi COSOMA.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media