Home » MR KAZIBWEZE SAMUEL WILLISON – BIOGRAPHY

MR KAZIBWEZE SAMUEL WILLISON – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
296 views

Mr Kazibweze Samuel Wilson anabadwira kwa T/A kuthembwe, kukulira komweko.Anabadwa pa 25 December 1989.M’banja mwawo anabadwa ana 8, ena anamwalira anatsala awiri ndipo iye ndi wa number 2.

Wakumana ndi mavuto ambiri anali munthu wonyozedwa kwambiri komaso anthu ankangodana naye.Anali munthu womvetsa chisoni, anali munthu wosowa kanthu, anthu ankamunena kuti sadzakwatira,sadzabeleka koma pano ali ndi mkazi ndi ana awiri, oyamba dzina lake Esther Mr Kazibweze ndipo Esther ndi oyimbanso.Anthu amkati Samuel alibe tsogolo, wanamizidwa zedi mabanja a anthu atha mu dzina lake.Anamangidwapo komanso kumenyedwa kumunamizira kuti waba ndipo makolo ake adali wodandaula kwambiri mpaka kulira
Koma inali nyengo yowawa zedi.Anadwala kwa thawi yaitali moyo wake ukadachoka koma Mulungu sadalore.

Mulungu anamupulumutsa ku imfa nyumba inamugwera koma amathokoza Mulungu. Chaka cha 2010 adayamba kuimba nyimbo koma thawi imeneyo asanayambe ku jambura nyimbo ndipo anayamba kaye kwaya kuti aphunzire zambiri.

Nyimbo anayamba kujambura chaka cha 2017 mu December komanso yekha amkadzifunsa kuti kodi Ambuye zikutheka bwanji kuti zitere,atatulutsa nyimbo yoyamba ya kazibweze anthu ambiri anadabwa ali kodi zatheka bwanji munthu uyu kuti akhale oimba komaso waluso chonchi,anatulutsaso nyimbo yoti Siya ntchimo, nyimbo imeneyi idavutaso kenako anatulutsanso nyimbo yoti Gwada upemphere idavutaso ndiye anthu adayambano kumupanga sport amamuyitana m’ma show ndipo amapita m’ma show ambiri.

Chaka cha 2021 anapanga show yake pa 26 September itafika tsiku la show yake zidali zomvetsa chisoni poti anthu amachitirana jerasi ku South Africa tsiku la show yake palibe anabwera kunali anthu ochepa, anthu oimba amzake ena anabwera ku show yake adalira zedi ndipo iyeyo anangochivomereza kuti zimachitika.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media