Home » MPHATSO HAJI BANDA – BIOGRAPHY

MPHATSO HAJI BANDA – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
334 views

Mphatso Haji Banda ndi oyimba nyimbo za Mulungu ndipo dzina la Banda ndi la amuna ake pomwe la Haji ndi la abambo ake. Iyeyu anabadwa mu chaka cha 1991 pa 27 July kuchipatala chotchedwa Bwaila mumzinda wa Lilongwe ku Malawi ndipo chipatalachi chimadziwikaso ndikutiso Botomu.

Munthuyu anabadwira mubanja la ana 5 akazi okhaokha ndipo iyeyu ndi omalizira kubadwa kubere lakwawo mtundu wake ndi mu yao kalero anali msilamu koma pano ndi khristu wa mpingo wa CCAP ndipo mtundu umenewu umadziwika ndi asilamu koma iyeyu anasiya chisilamu kutsatira amuna ake a Banda ku chi khristu.

Kumudzi kwawo ndi Ku Mangochi T/A katuli m’mudzi mwa Abwanali Makoli ndipo ali ndi ana atatu, atsikana alipo awiri m’nyamata m’modzi.Kuyimba anayamba 2009 ndipo kuchokera mu chaka chimwenecho anajambulako album imodzi imene inali ndi nyimbo 10 zoyambilira yomwe anajambula kwa Joh Mkhoma anayesetsa kuti nyimbo zake zifikire Madera ena ndi ena koma sizinafikire chifukwa chakuchuluka omupondereza zitatero sanatopebe anajambulaso album ina yokwaniraso nyimbo zina 10 nyimbo zimenezi anazajambulanso Ku studio kwa Antony Makuta kenako anayamba kujambula imodzi imodzi Ku ma studio osiyanasiyana mu nyimbo imodzi imodziyo munali ina anapangidwa feature ndi Ruth Missi anajambulanso ina anamupangaso feature born kavala Banda , kuchokaso pamenepo anapangidwa feature nyimbo ina ndi Kondwani Chirwa ndipo umo amajambula nyimbozo nkuti atakwana ma album awiri anayamba kujambula zoonera koma sizinamalizike pa zifukwa zina kotero zinathera panjira kenako anakhala chete kuchokera 2016 amangojambula nyimbo imodzi mwa apo ndi apo koma muchaka ichi cha 2024 ndipamene wadzukaso ndi mayimbidwe atsopano mwezi wa January ndipomwe anaganiza zoyambaso kuyimba ndikujambulanso nyimbo zina ku studio ina yotchedwa C.L Touch producer wake ndi Viwe Chibwana ndikomwe watulutsirako nyimbo ziwiri zomwe mitu yake ndi Chikhulupiliro ndipo yotsatira mutu wake ikuti Mukanena za ine,nyimbozi zatuluka kumapeto kwa mwezi wa March ndikomwe akuyembekezera kuti ajambule nyimbo zina zokwanitsa album yonse Ku C.L Touch Studio.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media