Jester Khembo anabadwa pa 01/08/1981 ndipo anabadwira M’mudzi mwamchakalima, T/A Tengani Boma la Nsanje.M’banja mwawo anabadwa ana okwana 5 iye ndi wa number 5 womaliza mzime ndipo onse alipo.
Atabadwa anapatsidwa dzina loti Job (Yobu) ndipo wakhala nalo dzina limeneri kuchokera ali wang’ono mpaka anafika pozindikira yekha.Anabadwa banja lopemphera makolo ake anali mtumiki wa Mulungu Zeka Khembo ndiye bambo ake,Mayi ake anali Tchai Khembo amene anamwalira pa 14 August 2014.Mpingo umene bambo ake ndi onse amapemphera unali wa Apostolic Faith Mission.
Kufikira 1994 anapita ku Lilongwe kwamtsiliza komwe anakayamba primary school yake, anakayamba pa Chigoneka Primary School standard 1,2 mpaka anapita pa Lilongwe L E A School, kenako anabwerera kumudzi 1997, anapita pa Phanga Primary School pamene anapitiliza Primary School standard 5 up to 8 kotelo kuti 2001 anasankhidwa pa Tengani ku Community Day Secondary School pamene anaphunzira form 1 mpakana form 3.2004 anabwereranso ku Lilongwe.Ali form 4 amkapita ku Chigoneka Community Day School pamene analemba mayeso ake 2004 amene sanachite bwino kotelo ndipamene anakumana ndi mzake Safuna anamuuza akuimba pa Asembly anamuyitana kuti apite ku church kwawo.
Sunday anapita limodzi kukapemphera ndipamene anayambira CCAP kuchoka ku Apostolic Faith Mission,kotelo kuti kuyambira pamenepo anabatizidwa ku CCAP kukhala mkristu.
2010 anapita kukabwereza pa Bwaila Secondary School form 4 anayimba ndipo anakumananso ndi mtsikana amene amakonda kuyimba Mphatso Chikuse amene amayimba ku Scom ndipo maimbidwe ake anakula kufikira 2013 pomwe anayamba kujambula nyimbo.
2014 anatulutsa album yake mutu wake Tiwapempherere atatelo 2016 ndipamene ananyamuka kupita ku South Africa.From 2016 anakhala akuimbabe,mu July 2023 ndipamene amapanga launch Woyera Mtima Album ndipo Album yake yachiwiri pano akujambula ma video kufuna kupanga DVD.