James Gulule ndi woimba,mtumiki (Evangelist) komanso mphunzitsi yemwe adabadwa pa 4 April,1992.Ndi mwana woyamba kubadwa m’banja la kwawo momwe muli ana 9 (amuna 4 ndipo akazi 5).Ndiokwatira ndipo ali ndi ana awiri (Roland komanso Angel Gulule).
Kuimba adayamba m’chaka cha 2002 kuchokera ku kwaya ndipo wakhalapo choir master kwa zaka 9. Kuimba payekha adayamba kuimba m’chaka cha 2018 pomwe adatulutsa nyimbo yomwe inkatchedwa Sindine Olephera, ndipo idakondedwa ndi anthu ochuruka omwe ankamvera Times radio pa nthawi imeneyo.Pano ndioyimba wokhazikika ndipo ali ndi masomphenya akulu zedi chifukwa kwa Iye kuimbaku ndi utumiki ndipo ali mkati mojambula Album yomwe ituluke 2024 August.
Iye adaitanidwa kukhala mtumiki (Evangelist) m’chaka cha 2019 mu mpingo wa CCAP. Ndipo akaitanidwa amatumikira m’maimbidwe komanso kulalikira mau a Mulungu pagome.
Pano ali ndi nyimbo ngati izi; Mdalitso,Vomera,mwandikondera,madalitso ndi zina zambiri zomwe zikutsitsimutsa anthu m’malo osiyanasiyana.
1 comment
Nice one Ambuye apitirize kuzala zazikuru mwainu nachulukise masiku amoyo wanu