Home » ISAAC CHIKOYA – BIOGRAPHY

ISAAC CHIKOYA – BIOGRAPHY

by Malawi Gospel Music
211 views

Isaac Chikoya anabadwa komanso kukulila m’mudzi mwa
Ulaya Mhone Village ku Endindeni Nkosana Yesaya Nkosi, TA Chindi ku Mzimba. Iyeyu anabadwa pa 17/04/1982 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 5 awiri amuna atatu atsikana ndipo iye ndiwanambala 3 pobadwa.

Atangobadwa adapatsidwa dzina loti Isaac , iyeyo makolo ake ndi achi khilisitu ampingo wa SDA monga tikudziwa dzina loti Isaac likupezeka m’bayibulo ndi mwana m’modzi yekhayo wa Abraham omupeza atakalamba kale ndi mkazi wake Salah ,ndipo likutanthauza kuti chisangalalo. Iyeyu adabatizidwa ali ndi zaka 13 ubatizo olowa m’madzi kumtsinje monga anabatizidwila Yesu Khilisitu ku mtsinje wa Yolodani.

Mayitanidwe amayimbidwe adamufikila ali wachichepere kwambiri, wayimba ku Sunday sukulu ku church kwaya, komano adayamba kupeka nyimbo zake mu 2000 ali ku secondary sukulu koma chifukwa chamavuto azachuma sanathe kujambula nyimbozo.Anaganiza zokasaka ku Joni m’chaka cha 2004 sanayiwale mayitanidwe ake ayi ndipo kuzafika 2010 ndipamene analowa mu studio koyamba kujambulitsa nyimbo ngati single yotchedwa Ndikhululukileni ndipo inafika pa radio Mzimba m’bomalo. Iyeyu ali pa banja ndipo adadalitsika ndi ana 4 wamamuna m’modzi,aakazi atatu,maina awo Abraham, Natasha, Ronna, komanso Jean, kukamba za dzina loti Chikoya lidabwera chifukwa cha m’pira , ali wachichepere amakonda kumenya mpila kwambiri moti ali talented ndi maluso ambiri . Adasankha dzina loti Isaac Chikoya lamayimbidwe.Ali ndi ma album awiri yoyamba Usapupulume yomwe adatulutsa 2015 komanso I have Jesus yomwe watulutsa 2020.

Spread the love

You may also like

Leave a Comment

malawigospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel Music and any gospel News.malawigospelmusic.com offer services like song lyrics,Audio upload,poems,Music video upload on our You Tube channel called Malawian Gospel Music, Artist biography, Extended playlist (EP),Article, Album and Banner on website. For inquiry contact these numbers 0888 069 117/0885 572 836 or 0983 592 032/0994 56 15 46 or info@malawigospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media