Hope Bonjesi anabadwa komanso kukulira ku Chikwawa M’mudzi mwa Buneta T/A Masache.Anabadwa pa 23/11/1992,ndipo ndiwoyamba kubadwa m’banja la ana anayi.
M’chaka cha 2013 anayamba kulemba nkhani zomwe amaziwerenga pa assembly ali ku Secondary pa Phanda Community.Mu 2015,anayamba kulemba ndakatulo ndipo 2021 anatulutsa ndakatulo yoyamba yomwe amati MUTIYENDERENSO M’BADO UNO UKUDZIWENI.Kufikira lero wajambula ndakatulo zokwana 9 ndipo zolemba zilipo zochuluka ndithu.