Evangelist Favoured Oprah anabadwa komanso kukulira ku Ntcheu M’mudzi wa Dambo. Anabadwa pa 07/04/1992 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 3 akazi okhaokha ndipo iye ndi wa number 2 pobadwa.Iye atabadwa adapatsidwa dzina loti Olipa lomwe likupezeka mu Buku la Rute.Kukamba za dzina loti Evangelist Favoured Oprah, lidabwera kamba ka Maitanidwe.
Maitanidwe amaimbidwe adamufikira mu chaka cha 2020 ndipo adayamba Kupezeka pa air mu 2021 pomwe adatulutsa nyimbo yoti Nthawi Yatha.Iye ali pa banja ndipo adadalitsika ndi ana awiri wamamuna ndiwamkazi ndipo maina awo ndi Vinny komanso Gianna.