Born on 07 july 1977 at Lilongwe Bwaira Hospital, Emmanuel Liwotcha ndi mwana wa bambo ndi mayi Liwotcha ndipo anakwatira Chikondi Munkhondya Liwotcha nayenso ndiwoyimba nyimbo za gospel, ali ndi ana 4 oyamba ndi mnyamata Alinafe nayenso amayimba ma drums komanso ndi oyimba, wachiwili ndi mtsikana Peace nayenso akuphunzira kuyimba, wachitatu ndi mtsikana Akuzike ndipo omaliza ndi mtsikana Mzati.Chokhumba chake ndikufalitsa uthenga wa Mulungu kudzera mukuyimba pa dziko lonse lapansi.
Emmanuel anaphunzira sukulu yake ku Chimutu Primary School ku Lilongwe kenako kwa mponda Primary School ku Balaka Secondary, anamphunziranso kwa Phalura Dec ndi St Louis montfort Dec ku Balaka ndipo anapanga course ya driving ndipo pano akungwira ntchito ku Enjoy Car Hire ngati Sales Marketing Manager.
Anayamba kuyimba mu choir pa St Louis Montfort Parish pa Balaka ali wachichepele ndi brother wake lsaac Liwotcha. Emmanuel anayamba kudziwika ngati solo artist in 2018 pamene anatulusa nyimbo ndipo zimamveka m’ma radio. Emmanuel anakulira ku Balaka ndi m’chimwene wake lsaac omwe amayimba mu Alleluya Band komanso Zembani Band.
Emmanuel wangwirako ntchito ku Imbilani Yahweh Studio komanso ku Zembani.Emmanuel ndiwa number 9 mu banja la ana 11 ndipo ana 4 anamwalira anatsala ana 8, ali ndi nyimbo monga Lipenga Lalira,Mutichitile Chifundo,Mutimvele komanso Muyende Nane.Emmanuel ndi Khristu wa Anglican ndipo ndi lay leader ku mpingo wa ku Christ The King Anglican ku Benito ku area 23 Lilongwe under Chilinde Parish ndipo ali ndi producer amene akujambula album ndi Sir Evance Watsopano Meleka ndipo pakutha kwa chaka chino album imeneyi ikhala ikutuluka.