Chrispine Chaoneka nde dzina lake lapamsonkho koma lapa stage ndi EL DEEZ.Khili adabadwila ku Lilongwe, likuni hospital pa 18 February 1985 ndipo ndiwachiwili kubadwa m’banja la ana atatu.Oyamba kubadwa ndi Francis ndipo omaliza ndi Beatrice Chaoneka.
Khili wakhala madela ambiri monga ku Mzuzu, Blantyre, Karonga komanso Zomba.Sukulu adapita ku St Patrick’s Secondary School komanso Nasawa Technical School koma amapanga zau mechanic koma sadapitilize.Nkhani yamayimbidwe adayamba ali mwana komanso kumveka pa radio adayamba ali mwana pamene ankapanga program ya ANANU TISEWELE pa MBC radio 1.
Wayimbapo m’makwaya monga Chinsapo Church Choir komanso Chinsapo Youth Choir ku CCAP.Khili amakhalira ku South Africa ndipo ali pa banja anadalitsika ndi ana awiri a boy and a girl.
Nyimbo zake amajambula ku malawi ku Real Sounds Studios ya Skeffa Chimoto ndipo producer wake ndi Apex.