Davie Nahawa anabadwa komanso kukulira m’boma la Zomba, m’mudzi wa Ramusi Mfumu yaikulu Mwambo.
Iyeyu luso lake linaonekera ali mwana maka Ku Sunday school komwe anali m’modzi mwa ana oimba bwino kufikira magulu akulu akulu pa mpingo anayamba kumutenga kumathandizira kuimba m’mipikisano mu Blantyre Synod.
Kufikira panopa chidwi chake chinakula ndipo akuthandizira ana amene akuimba komanso kuchita maluso osiyanasiyana okhuza Mulungu.
Pakadali pano ndi Director wa Chinamwali CCAP Sunday School Choir yomwe ili boma la Zomba komanso Mpachika CCAP Sunday School Choir yomwe ili Ku Blantyre.