Chosen Man anabadwa pa(6/9/1992 ndipo kumudzi ndi ku Phalombe koma anabadwila ku M’chinji komwe kunali makolo nthawi imeneyo koma pakadali pano akukhalira ku Johannesburg m’dziko la South Africa.
Atakulako msinkhu from 2008 ndipomwe maitanidwe awutumiki anabwela kudzela ku maloto, amalota akuimba pena akutumikila izi zimachitika kwa nthawi yaitali kufikilaso pomwe anabatizidwa 2011 apa anapitiliza kulota ndipo anali okakamizika kutumikila Mulungu kenako anapezako mwai otumikila nao pa mpingo wina.
Kuimba kunayambika 2022 mkuti atakakamizikanso kutelo apa ndi pomwe panabwela dzina la Chosen Man.Dzina lomwe anapatsidwa atabadwa ndi Gift Sonkhanani.