Camillius Simakweri anabadwila ku chileka m’boma la Blantyre ndipo anakulira ku Zimbabwe komwe anachita maphunziro ake a primary.Banja la kwawo anabadwa ana atatu ( kumbali ya amayi )ndipo ana 5 ( kumbali ya abambo)
Anabadwila ku banja la mayimbidwe chifukwa bambo awo a Patrick Simakweri komanso mkulu wawo Sam Simakweri ndi m’khala kale ku nkhani yamayimbidwe ku malawi kuno.Anayamba kuyimba m’chaka cha 2010 ali achichepele pomwe iwo ndi anzawo ena Laurent ndi Andy Phiri anayambitsa gulu lotchedwa evergreen gospels ,guluri linatulutsa single imodzi yotchedwa amatelo nanga? ndi malemu William Kwiliyo,nyimboyi inachita bwino mu chart ya radio 2 komanso CFC radio,pazifukwa zina Laurent ndi Andy anatuluka muguluri ,koma Camillius anapitiliza kuyimba muguluri ndi nzawo wina Thoko Phiri.Guluri linatenga mbari mumipikisano yambiri monga crossroads ndipo linachita bwino ngakhale kuti anali ana achichepele nthawi imeneyo.M’chaka cha 2012 Camillius anatulutsa chimbale chake chomwe chinajambulidwa ndi Mvahiwa Hanke ku Audio Clinic,anatulutsanso ma single ena ndi ma producer ena monga Petros Chingoma komanso Thocco Phiri.Atakumana ndi zovuta zina anaganiza zosiya kuyimba m’chaka cha 2017 koma m’chaka cha 2022 anaganiza zoyambilanso kuyimba.Anajambula ma single awiri,Mwari wangu ndi koma yesu ameneyu ndi princo ku Dynasty Studios m’boma la M’chinji komwe anakhazikika pano.